Dowa District Council

Dowa District Council

Share

Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Dowa District Council, Public & Government Service, Dowa District Council, Private Bag 2, Dowa.

Photos from Dowa District Council's post 31/05/2026

BUNGWE LA LET'S BUILD LIPEREKA MA KALASIRUMU BULOKO KHUMI NDI ATATU KU BOMA

Pachiweru, bungwe la Let's Build Foundation - Malawi lapereka ma kalasirumu buloko khumi ndi atatu ku unduna wa zamaphunziro, omwe amangidwa mma sekondale sukulu oyendera (CDSS) asanu ndi awiri m'boma la Dowa.

Mabulokowa amangidwa mma CDSS awa; Kawangi, Nalunga, Simbi, Chimwetsero, Chakhadza, Mdika komanso Tchale.

Nduna yoona zamaphunziro a Bright Msaka, SC, ndi amene analandira makalasirumu bulokowa mmalo mwa boma, pa mwambo omwe unachitikira pa Simbi CDSS mdera la mfumu yaikulu Dzoole.

Iwo athokoza bungweli ponena kuti izi zithandiza kutukula maphunziro m'boma la Dowa. A Msaka atsindikanso kuti boma ndilozipereka kutukula maphunziro, ndipo lionesetsa kuti mmasukulu a sekondale onse muli zipangizo zoyenera zokwanira.

Mkulu wa bungwe la Let's Build Foundation - Malawi mayi Ruth Kamwendo anati ndi cholinga chawo kuthandizira boma kuti ophunzira aliyense athe kukhala ndi kalasi yophunziliramo, ndi cholinga choti maphunziro afikire kwa mwana wina aliyense.

Mabulokowa ndiokhala ndi makalasirumu awiri iliyonse, komanso akudza ndi ma desiki makumi asanu (50) mu kalasi iliyonse.

Bungweli laperekanso zimbuzi khumi ndi zinayi mmasukulu wa, zomwe ndizofikirika kwa ana a ulumali, komanso zokhala ndi zipinda zosinthira za atsikana.

"Tikulengezanso kuti timanganso ma buloko ena ngati amenewa, awiriawiri pa sukulu za Mbalame, Chibanzi komanso Kaungwe," anatero a Kamwendo.

Wachiwiri kwa wapampando wa khonsolo ya Dowa khansala Lenard Kafumbula wapempha ophunzira kuti alimbikire maphunziro awo.

30/05/2026

On a lighter note -
Congratulations PSG - Paris Saint-Germain
Anthu agone. Pang'onong'ono tinakamvanso kuti akufuna kuyenda mu Dowa mu kukondwelera chikho lol.

21/05/2026
16/05/2026

Malawi News
May 16 - 22.
Uthenga ku ma area.

15/05/2026

Auzeni akutsalirawo apange follow Dowa District Council

14/05/2026

Happy Kamuzu Day!

Photos from Dowa District Council's post 13/05/2026

Bwanankubwa wa boma la Dowa James Kanyangalazi wapempha anthu mb'omali kuti achilimike poonesetsa kuti akukhala kapena kugwira ntchito mmalo aukhondo ngati njira imodzi yopewera matenda.

Iwo alankhura izi lachitatu pamene khonsolo ya Dowa inakonza mwambo osesa ndi kuchotsa zinyalala, kuchokera ku ma ofesi a khonsoloyi kufikira ku nsika waukulu wa Dowa.

"Ndi udindo wa aliyense kuonesetsa kuti malo amene tikukhala ndi aukhondo. Ukhondo ndi njira imodzi yopewera matenda.

"Anthu akakhala ndi thanzi labwino, atha kukhala ndi nthawi yotukura mabanja awo komanso kutengepo gawo pa ntchito zotukula dziko," anatero a Kanyangalazi.

Wapampando wa khonsoloyi khansala Billy Mtika anati khonsoloyi ipitiriza kufikira madera ochuluka mb'omali ndi ntchito ngati imeneyi.

Wapampando wa komiti ya nsika wa Dowa bambo Oliver Katema alonjeza kulimbikitsa anthu mu nsikawu pa ntchito zaukhondo.

Anthu osiyanasiyana monga ogwira ntchito ku khonsoloyi, ku chipatala chachikuku cha Dowa, ochita malonda, anthu a mdera ndi ena ambiri anatengapo mbali pa ntchito yi.

Khonsolo ya Dowa ikugwira ntchitoyi pansi komanso motsogozedwa ndi Executive Order number 2 of 2026, yomwe ikulimbikitsa ukhondo.

13/05/2026

Sweeping Exercise

13/05/2026

Grand Clean-up Exercise!

12/05/2026

It is everyone's responsibility to keep Dowa clean!

Want your business to be the top-listed Government Service in Dowa?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Website

Address

Dowa District Council, Private Bag 2
Dowa