Ali Liz's Library

Ali Liz's Library

Share

Nkhani za nsangulutso zosiyanasiyana komanso zophunzitsa

15/06/2026

THE MANIPULATED QUEEN

Chapter 128

Onse anali atakhala pasi koma akumuyang'ana Stella uja. Ana okha ndi amene anasazika nkumapita kukagona.

"Mother you could have told us. Osati kutizizimutsa."
"As if mukanakhulupila." Anatero Lydia. Anali atawafotokozera chilichonse mene zinthu zinakhalila.

Ena anali ndimafuso koma anangosankha kukhala chete.
"How can you fake your death Stella? Tinayendesa mwambo onse yet you were alive and breathing?"
Stella anawayang'ana ankolo ake amene amawoneka kuti anali atayamba kukalamba.
"I had no choice. "
"What do you mean ukamati panalibe choice!"
"Don't shout."
"Why shouldn't I? Now aliyense aziti wauka kwa akufa. Mwambo unachita kuyendesedwa. And everyone saw everything. "
"I will clear everything out. Ndikati I had no choice. I really did."
"Ndimadziwa kuti utha kupanga zinthu zonse koma osti kutipusisa akulu akulu ife."
"She said she had no choice. Ndiye ukufuna kuti afotokoze chani? And wanena kuti apanga explain chilichonse so live it like that." Lydia..
"Ndife akulu akulu. She was not supposed to do this to us."
....

Pamene masiku a will anali atadusa Solo anayamba kumakwanisa kumva thupi lake mosiyana ndi mwanthawi zonse.

Anali atachosedwa kunyumba imene ankakhala ndi Jessica koma akukhala ndi Arena.

Arena anali atakhala pa mpando akumuyang'ana Solo uja.
"Ukuziwa sindikuziwa kuti what happened to you." Anatero akumuyang'ana nchimwene wake mwachidi.
"One day you were fine the next day wagwidwa ndi stroke. What happened brother? Whom did you wrong? Because it doesn't make sense." Anatero kenako anapumira mwamba.

Solo anasuntha mwendo koma Arena sanawone koma Solo anali atawona. Anayeseranso kuti asunthe mwedo wake koma zinakanika.
"Anyway, am here to tell you about your divorce. It was successful. Jessica anapempha zinthu zingapo. Ndinakumana ndi sister wake and we finalized everything...."

Anakhala kanthawi ngati akuganizira.
"You know am happy kuti wasiyana naye but am sad kuti uli chonchi. Don't worry your niece akabwera azikuchezesa. Ndikukhulupilira kuti lero sukulu akuonako kuchedwa kuti aweluke. She loves you. She really dose."
"Are.......na"

Arena anayang'ana chipinda modabwa ndipamene amazamuyang'ana Solo.
"Did you just speak?"
Solo anamuyang’ana.
"You said my name. I believe I heard you."
"Are...."
"Solo!"

Anagwira pakamwa ngati alili.
"You are speaking!"
"Na..."

Anayesera kusuntha thupi lake ndipo zinatheka.
"Solo!"

Anatuluka nchipinda muja mwachangu. Anakatenga foni yake nkuwayimbira adokotala kenako anayimbila bambo ake.

Pamene bambo ake amafika nkuti dokotala atafika kale akumupanga check Solo uja.
"Zikuonetsa kuti pali kusintha kwa mankhala amene amapasidwa and akuonetsa kuti mankhwala amenewo ndiamene akumuthandiza."
"Ndiye bwanji mbuyo monsemu samapasidwa?" Anafusa bambo ake.
"Chifukwa some medicine can react negatively to someone but positively to others and at the same time others are neutral they don't show any sighn. Mankhwala amene amapasidwa ndi amene akhala akuthandiza anthu osiyanasiyana koma to him zinali zovuta."
"Chabwino doctor. Koma akhala bwino?"
"He will surely be fine. "
"Ndimankhala amenewa. Zitenga nthawi yayitali bwanji?"
"2 to 3 weeks kuti akwanitse kulankhula. Adding to that azipita kokawawongola."
"He does that."
"Then kwinako sizivuta. Ngati zatheka kulankhula after 2 days. Kwinako sizivuta."
"Okay."
"I have to go. Kwinako azimalizisa nurse uja."
"Tathokoza doctor."

A doctor ananyamuka nkumapita.

Arena ndi bambo ake anamuyang’ana Solo.
"You will be fine son."
"Yes he surely will."
....

Mbali ina Molly zinthu zinkamuyendera kwambiri.

Kulumikizana kwa iye ndi Zack kunafika pokoma kwambiri moti amamuza chilichonse. Mene siku lake layendela komanso antchuto amene anamukwiyisa.

Tsiku lina Zack anamutengera kunyanja koma dela limene kunalibe anthu ambiri.

Anakakwera boti limene mumakwera anthu atatu. Iwo ndi driver oyendesa. Dzuwa linali likuwala nthawiyo nkuti boti lija likuyenda pakati pa nyanja.

Anali atayima mphepete mwa boti kwinako Zack akumunong'oneza Molly.
Molly anaseka kenako analoza nsomba imene anayiwona.
"You are silly. Ukukuwa ngati nsoba sunaiwonepo bwanji?"
"Isn't it cute? Sindinaonepo nsomba ikusambira."
"Do you think ikusambira?"
"Ndiye ikutani?"
"Ikuyenda."
"No ikusambira mesa ili madzi."
"Madzi ndi media yake kaya."
"Koma madzi timatani mesa timasambila."
"Chabwino Chabwino eya ikusambira."
"Ndiye bwanji umanditsutsa?"

Zack anayima kumbuyo kwake.
"Ndi ngatsutse the mighty queen?"
"Am the queen now?"
"Yes of my heart, my head, my body in fact everything."
"That's sweet of you."
"Yes."

Anapitiliza kukamba nkhani zawo kwinako akumalozeraba zinthu.

Comment....

15/06/2026

THE MANIPULATED QUEEN

Chapter 127

Analinali akuyang'ana nsapato zoti avale. Rod anali akuvala shati yake koma akuyang'ana zimene Stella amachita.

Anatenga nsapato zake ndikuvala kenako anakayima pa mirror kuti akonze tsitsilake. Rod anakayima kumbuyo kwake nkumamuyang'ana kuzela pa mirror paja.

Anatenga zimene zinali patebulo zokongoletsa mutu ndikuvala.
"I married the most beautiful lady."
"We are not badies."

Rod anamwetulira akumuyang'anabe koma Stella anali akupanga zamutu mwake.
"After what we did?"
"We did what?"
"Stella..."

Anamuyang’ana maso kuzera pa mirror paja.
"I thought ichi ndichiyambi chathu chatsopano."
"Your thoughts not mine."
"Why are you being difficult?"
"Am I?"

Anatsegula mene mumakhala ma jewelry ndikutenga necklace. Anasankha imene inamusangalatsa. Anatenga kuti aziveke koma Rod anagwira nkono wake.
"Let me do it for you." Anatero atagwira nkono wake.
"Alright."

Anamuveka koma pang’onopang’on.
"Are you scared?"
"For?"
"Anthu akuziwa kuti unamwalira. Somewhere there is a tombstone Stella."
"To answer your question. Am not and zinazo ndithana nazo ndekha it's not a big issue. "

Atamaliza kumuveka anamutembenukira ndipamene Stella amawona kuti Rod anali atasemphanisa mabatani.
"Umavala ukutani?"
"Ndatani?"

Anayamba kumumasula mabatani aja. Rod anamwetulira.
"This doesn't happen regularly."
"Umatere?"
"It’s because I was looking at you."
"Ndiye mpaka kusephesa mabatani?"
"It’s because I feel like am dreaming."
"Ndaonanso."

Anamaliza kumumanga mabatani aja.
"I will be with you in everything."
"We will see."
"Trust me."
"Let's not speak about that."

Anamwetulira mozikakamiza kenako Stella anasuntha nkukatenga zinthu zina.
"I miss my daughter. Komanso I think it's time to go?"
"Are you sure?"

Stella anayimika zimene amachita nkuzamuyang'ana Rod.
"Ndikuoneka wamantha?"
"No..."
"Ndiye?"
"Ndimafuna ndikuziwise kuti just in case uli ndimantha. Am here."
"Ndakumva."

Anatuluka nchipinda muja.
...

Anthu amanong'onezana maka zokhuza mwana amene amawoneka ngati Stella. Anali manja mwa Lydia komanso amawoneka kuti akukambilana. Mwanayo amafusa mafuso.

"Akuoneka ngati Stella ali mwana."
"Kapena mwina Stella anali ndi mwana penapake?"
"Kaya. Angaziwe zimenezo ndani?"
"Ndiye tiziti tabwera kuno tikuzatani?"
"Koma kamwanako ndikandani."
"Ineyo ndikuona ngati chinachake sichilibwino. Ndikukhulupilira anthunso akukamba zomwezi. Mwanayo ndi ndani?"
"Mwina umufuse Bella atha kuziwapo kanthu. Paja amaziwa chilichonse chokhuza Stella. Usaiwale ndiyeyunso ananena zokhuza ka company akuti akukayika kuti ndika Stella."
"Wangosowa oyambana naye. Pano anadekhatu."
"Osati chifukwa cha mimba imene alinayeyo?"
"Ndakayika. Mwina atha kukhala mamuna wake uja."
"Wabwera kodi? Sindinamuonetu."
"Ndani? Quinn?"
"Eya, Bella ali yekha."
"Sizingatheke Quinn kumusiya ekha. The way that man adores Bella. Kuyambira ali bodyguard amwene."
"Ndiye timakamba za kamwanako. Nkhani ya Bella inanditopesa. You know there's nothing interesting again in this house. Nthawi ija Stella amabebetsa amwene. Amati akamalowa wekha umachita kuziwa kuti kukubwera namondwe. Ndiye naye Bella amazayipasa moto."

Anayamba kuseka koma akunong'onezana. Bella anali akuseweresa foni yake pamene mamuna wake amafika nkukhala pambali pake.

"You see. I told you. Quinn sangamusiye Bella. Kulikonse amayendera limodzi anthu awa."
"Koma nyamatayo ee wapilira. Mene Bella ankhachitila? How did he do it?"
"Mwina nchikondi. Muziwa bwanji?"
"I remember tsiku limene anakangana ndibera lija. Do you remember?"
"La birthday yake lija?"
"Limenelija eeee. Quinn anakwiyatu. Ndipo akanati akhale pa birthday imene ija. Akanapha mwana wa munthu."
"Bella ananyanya nakha munthu akamunyoze chonchija? Ndiye pagulu. Ngati chipsyeracho chinabwera chokha? Chinabwera chifukwa he saved here."
"Eti inu. Now look at them. Together again. She tried to push him koma zinakanika."
".... mmm ndikumva kuzizila choncho. Ndichifukwa chani temperature yatsika?"
"Temperature itsika bwanji kanthawi komweka nawe?"
"No... am not wrong I know this feeling."
"Which feeling?"
"This is not strange..."

Ndipamene anamuona Stella.
"Mimi, can you slap me please. "
"Vuto lako ndichani?"
"Just give me a big slap imene sunapasepo munthu."
"And your children will say what?"
"A ghoooooooost!!!!!" Anatero wkuloza kunali Stella kuja.

Anthu onse anachewukira kumene kumatulukira Stella. Eeee ana kunali kuthawa. Azibambo anayimilira pamene azimayi ena anathawila nzipinda zawo.

Nyumba monse munali chipwilikiti. Ena kunali kukolana nkugundana.

Comment....

11/06/2026

THE MANIPULATED QUEEN

Chapter 126

Rod anapanga njira yoti akumane ndi Lydia ngakhale zinali, zovuta kuti akumane naye.

Anali akumudikira kuti nthawi iliyonse afika. Sipanatenge nthawi anafikadi.

Anali akuyenda pang’onopang’on koma akugwilitsa ntchito n'dodo. Anafika ndikukhala pa mpando.
"The Jere man."
"Mulibwanji mai Fyson."
"Am good as you can see me. Iweyo ulibwanji?"
"Sindilibwino chifukwa cha chizukulu chanu."

Lydia anamwetulira.
"Don't use parables with me Rodney. Ndakula and I don't have time to guess and do other stuff. Ukuziwa kuti ndili ndi zizukulu zingati? Be specific."
"Stella." Anatero akumuyang'ana Lydia.

Lydia sanawonetse kudabwa kulikonse.
"Stella? What about her? Ukufuna ukwatile? You know ifeyo, we don't have a problem with you getting married again?"
"Ndikudziwa koma your granddaughter is alive."

Lydia anasamila mpando akumuyang'ana Rod ngati wabalalika.
"It’s 6 years."
"Ndikuziwa."
"I can't stop mourning my granddaughter ndiye usandipangise kuti ndikumbukire zimene I want to foget. Stella was my favorite daughter."
"Am sorry koma believe me that Stella is alive. All this years wakhala akuzibisa. She fooled us."
"Stella sangapange zimenezo."

Anatenga foni yake nkupita kuzithuzi. Anawawonesa zithuzi zimene anatenga Stella akuchita zina. Lydia ataona anayendesa nkono wake pa chithuzi chija.
"She has a child?"
"Yes."
"Yours?"
"Yes she is mine."
"What's here name."
"Lisa."

Anali asakukhulupilira. Patapita kanthawi ndipamene amazindikira kuti chikuchitika ndi chani.
"Why did she hide?"
"Because of me I guess."
"Ndiye ukufuna nditana? This place kumene akukhala sikunandisangalase. Akuyenera kuchokako."
"Exactly my point."
"We are going today kukamutenga."
"Okay."
"Can you excuse me for some time. I want to make a call."

Anavomera ndikuchokapo. Lydia anamuyimbira foni Lucas.
"Hello?"
"Undiuza chani zokhuza Stella?"
"What do you mean?"
"Ali moyo?"

Lucas anakhala chete kwakanthawi.
"Eya."
"For how long Lucas?"
"After myezi itatu malilo atachitika. And I met her."
"And you said nothing?"
"She wanted me to be silent."
"Bwana wako ndi ndani kodi?"
"Ma'am Lydia, my job was to work for Stella. I have done that mpaka panopa. Am still doing what I was employed for."
"Koma who employed you?"
"You ma'am."
"And unawona kuti ndikofunika kuti usandiziwitse za nkhani imeneyi?"
"Am sorry I didn't but even nthawi ikanabwerera, I will still do the same."
"You are fired Lucas."

Lucas anatengana nthawi koma akuganiza.
"Am sorry koma I can't be fired now. Stella is still operating in the system. You heard about Stalisa group?"
"What about it?"
"Ndiyake."
"Stella had the gut kundiyenda pasi?"
"It’s for her daughter. Not hers. Her reasons was that Akron belonged to a group of people. Samafuna kuti Lisa azapangidwe involve ndi politics ya ma Fyson."
"Am going to deal with her. How can she?"
"Am sorry."
"Well, arrange everything. Tikukamutenga lero. Invite everyone from our side. Don't tell them anything."
"Nditelo. Inuyo just be prepared. After an hour chilichonse chikhala chatheka."
"Okay."

Anadula foni akuoneka kuti alindimafuso. Anatapita pa internet nkufufuza za company imene inali ikuyamba kutchuka.
"I new something was off. Company singagwile nsewu mwachangu choncho unless there's someone behind this."

Anayimilira nkulunjika kuchitseko. Atatsegula anakumana ndi Rod.
"Thanks for telling me."
"She is my wife too."
"Tikhala tikunyamuka within an hour. Kakonzeke."
"Chabwino."
"Tionana."

Anasiyana kuti aliyense akakonzeke. Ola litadusa anakakumana ndi Lucas amane anali ndi ma bodyguards anagapo. Anali pa bwalo la ndege.

Anamudikira Lydia kuti akwere kaye kenako enawo anakwera. Ndege ija inayamuka nkumapita.
....

Pamene amafaika Lydia anali atakhumudwa maka ataziwa dela limene Stella anazibisa. Sanayembekezere mpaka pamene amafika.

Anthu amudzi anali akudabwa ndi magalimoto amene amadusa mudzi mwawo moti ana anthu ambiri anayamba kulondola magalimoto aja.

Atafika pa restaurant paja. Rod anakakumana ndi a Phiri pamene Lydia analowa mu restaurant muja nkumaponyaponya maso ndipamene anamuona Stella.

Anayenda pang’onopang’on mpaka anafika pamene anayima. Ntima wawo umagunda mowilikiza. Anamugwira saya kuti asimikizedi.
"Stella?"
"He bought you here?"
"Ulimoyo Stella?" Anafusa mpaka misozi inatsika masaya mwawo.

Nthawi yonse samakhulupilira koma atamugwira ndipamene anasimikizadi.
"Granny?"
"Why Stella? This place? You don't belong here. Why?"
"Khalani pasi."

Anawakokera mpando kuti akhale. Lydia kuti amusiye Stella zimakanika koma anakhala.
"Why?"
"I wanted to be far from everything. I was tired and ndimafuna malo amene ndingapeze ntendere."
"Ukananena koma not faking your death. People will talk. The world knows that you are dead."
"Ndikuziwa."
"How can you do this. If it was the space you wanted ineyo I could have arranged that. You don't know what your death did to us. The family was scattered. No one was interested to come to the Fyson house even at my birthdays. It was quite Stella. The family loved you. I know they hated you koma anthu amabwera chifukwa you where there."
"It’s doesn't change anything to me. I needed this to clear my mind and start again."

Lydia anamuyang’ana nkuzamwetulira.
"Unachita motani?"
"It’s a long story."

Anavomera kenako anayamba kuyang'ananso mu restaurant muja.
"Ndimalo a ndani?"
"Amene akhala akundisamalila zaka zonsezi."
"So it has your memories?"
"Yes."
"Am going to change everything. This place will be changed. Ndaona zinthu zingapo zimene zingapangitse anthu azibwera kuno. I want this place and this restaurant to be on the map."
"That's good."

Ndipamene Rod amalowa. Anaphana maso ndi Stella.
"Mwana wako ali kuti?"
"Kunyumba."

Anayamba kukambirana zina mpaka anapita kukakambirana ndi banja la Aphiri. Anavomelezana kuti Stella anyamukatsiku lomwero.

Amene anakatenga zinthu za Stella anali Rod. Stella anali atalongeza kale zinthu za Lisa ndiye sizinavute.

Atasazikana ndi anthu akuderako ananyamuka nkumapita. Ngakhale akulu akulu ankadandaula chifukwa chakuchoka kwake.

Lydia anali akucheza ndi Lisa nthawi yonse pamene Stella ndi Rodney amangoynizana ngati akufuna amenyane mundege muja.

Anakafika ku nyumba ya Lydia koma sanalowere khomo lalikulu. Analowera chitseko chimene sikumadusa aliyense.
"Chipinda chako ndimene unachisiyira everything is there. You can go with your husband. Ine ndimusamalila Lisa. Came to the table after 3 hours. Zovala akubwereserani Lucas especially za mwamuna wako. Zako kuchipindako zilipo. Zimasinthidwa mwezi uliwonse just the way you liked it."
"Okay."
"Kakonzekeni and rest for some time. Akubwereserani chokudya mukudikira nthawi ya supper. Lisa come and play with granny."
"You are my granny?"
"The real one my baby."
"I like you granny." Anatero akulunjika kukorido ina.

"Uzangoyima?" Anafusa Rod.
"You won."
"I always do."
Anamuyang’ana kenako anamudusa nkumapita kuchipinda chake.

Atafika anayamba kuonaona zinthu nchipinda muja. Anali atazikonzadi mene iye ankakondera. Mitundu yake inali yomwe ija.

Anamalizila nkuyima pa window. Ndipamene Rod anakayayima kumbuyo kwake.
"Ukufuna chani Rodney?"
"You don't love me anymore."
"At least I didn't have to say that aloud. Choka kumbuyo kwanga."
"Why? Am I affecting you?"
"Just move aside."
"Let's take a bath together."

Stella anamutmbenukira nkuzamuyang'ana.
"I missed you."
Sanamuyankhe malo mwake amangomuyang'ana.
"I know you can't forgive me. But I know there's tension between us. Fire and desire. Wakhala ukundiyang'ana munsewu monse."
"I was just thinking on how to get rid of you."
"Ndiye wapeza solution? Because I know. You found none."
"What makes you to be sure?"
"Because I know what you want. I can read it?"

Anathawisa maso ake nkuyang'ana kumbali ndipamene Rod amamwetulira. Anamuyandikira kwambiri pamene iye anabwerera mbuyo.
"Don't mess with my mind Rodney."
"Am I?"
"Stop it."

Rod anayima koma akumwetulira chifukwa ankamuziwa nkazi wake. Ma emotions ake akuadzuka pakamozi amamubalalisa ndiye amaopa kuti atha kumukankha iye nkutuluka. Anamupatsa nthawi kuti azitolere.

Anabwerera mbuyo koma muntima ali okondwa.
"You have not changed."
"What do you mean?"
"That's my secret to tell."

Pakhomo munthu anagogoda kenako analow ndichokudya.
"Ndabweresa chokudya." Anatero munthu uja akumuyang'ana Rod koma sanamuone Stella chifukwa anali atayima kumbali.
"Utha kuyika apo."
"Chabwino. "

Anakasiya chokudya chija kenako anatuluka.
"Kasambe Stella kenako upume. Ineyo ndikhala ndili panjapa mpaka umalize. Then I will take my bath."
"Alright."

Rod anatuluka nchipinda muja. Ndipamene Stella anapita kubafa kuti akasambe.

Anatsegula shawa nkumasamba. Anali akuganiza zochuluka.

Panadusa mphindi zingapo ndipamene amazindikira kuti kumbuyo kwake kuli munthu. Ntima wake unayamba kugunda mowilikiza. Munthu uja anayamba kumukisa mkhosi. Thupi lake linazizwa mpaka akanateleleka koma anagwidwa mwachangu.
"Are you going to resist me again Stella?"
"I shouldn't have trusted you."
"Not to a hungry man wifey."
"Leave me alone."
"Are you sure ndizimene ukufuna?"
Anamutembenuza kenako anayang'anizana.
"I missed you." Anatero Rod motanthauza.
Stella anayika nkono wake nkhosi mwa Rod ndikumukokera pafupi ndi iye. Madzi anali akuwathira onse.
"You are using a wrong strategy." Anatero akumunong'oneza.
"Undithamangisa?" Anafusa Rod naye akumunong'oneza Stella.
"Not now."
''You need me?"
"I do."

Anayang'anizana kenako anayamba kukisana madzi akuwathilabe. Rod anamunyamula Stella. Anatulika ku bafa kuja. Anamugonesa pabedi.
"I missed you wifey."
"Me too husband." Rod anamwetulira nkukwerala pabedi.

Comment....

11/06/2026

THE MANIPULATED QUEEN

Chapter 125

Malo molongeza zinthu zake zonse anatenga zinthu zochepa.
"Ndiye katundu wako wina ukumusiyila ndani?"
"This is my house."
"Nyumba yake iti?"
"Wandimva"

Anatuluka nkumenyesa chitseko mwa mphamvu. Arena anayang'ana chitseko chija asakukhulupilira.

Anamuyang’ana Solo amene amawoneka kuti anali akumuyang'ana.
"Look at you Solo. Why all of this? What happened to you?"

Anamumvela chisoni mbale wake kenako anakhala pampando. Foni yake inayitana ndipo sanachedwe kuyankha.
"Father?"
"Ali bwanji?"
"He is not okay. Hule lija ndalithamangitsa."
"Arena... just help your brother. Let the girl go and mumpatse zimene akufuna."
"Chani? Father that's not happening. Anabwera ndi chani pakhomo pano? She came with nothing so shall she live with nothing. Dad he left my brother ali chonchi? Why?"
"To avoid chilichonse. Mpatseni zimene akufuna. Don't waist your time pazinthu zosathandiza. Apa I was talking to their lawyer. He explained chilichonse to me and ndikuona kuti the best way is for him to come home."
"Why are you giving her zimene akufuna."
"Don't forget they have been together for years. She supported him mbuyo monsemu until now."
"Amayenera akhale nayenso panopa."
"Don't force someone zinthu zimene iye akuona kuti sazikwanitsa. She help at least. Sitikudziwa kuti Solo apeza bwino liti. It can be days, weeks, months and years. And Jessica is still young."
"Father she vowed."
"Remember vows can be broken."

Anamuyang’ana Solo.
"Okay, ndionesesa kuti chilichonse chitheke."
"Good. "
"Tilankhulana nthawi ina."
"Chabwino."

Anadulafoni nkupumira mwamba. Sipanatenge nthawi kunalowa nurse amene amamuthandiza Solo.
"Unali kuti nthawi yonse?"
"Ndimakumana ndi munthu amene amayenera kundipatsa mankhwala."
"Usamatalikire. He really needs your help."
"Okay."

Nurse uja anapita kuchipinda chimene anamupatsa akafuna kofikira. Anakasiya zipangizo zake malo oyenera. Analongeza zinthu zake nkuzipitisa kuchipinda cha Solo. Atafika anapita kumene kunali Solo.
"Akuyenera kuti akapasidwe mankhwala."
"Okay."
"I will need you help. Mugwile wheelchair yo."

Anamukhazika pa wheelchair nkupita naye kuchipinda chake.

Nurse uja anapanga connection chilichonse malo mwake. Solo anayang'ana botolo la mankhwala limene linali lachilendo. Amafuna asunthe koma zimavuta.
"Akungofunika nthawi yokwanira."
"Achila liti?"
"Ifeyo we are trying what we can koma akhala bwino."
"Okay."

Anamufundisa solo chofunda kenako anatuluka nchipinda muja nkupita kuchipinda chake.

Solo kuti ayang'ane zimavuta.
"You want to sleep. Just sleep brother. Everything will be okay."
Anagonadi Arena akumuyang'anira.
...

Ngakhale Molly samafuna zoyendayenda. Anatengana ndi Zack nkupita kumene amafuna kuti apiteko.

Molly anayang'ana dela lija nkuzamuchewukira Zack.
"Basi?"
"Basi chani?"
"Zack wandichotsa kuntchito nkundibweresa kuno? Kunoko? Of all places?"
"Kwatani kuno? This is a good place?"
"Ukufuna mawa dzina langa likhale paliponse? They will say we are dating."
"Are we not?"

Molly anayang’ana anthu amene amawayang'ana mwachidwi ena anali akutenga zithuzi zawo mobisa.
"This place is public. Aliyese azilankhula mene akufunira."
"Ndikunyanja kuno Molly, relax."
"How can I relax?"
"Look at me." Anatero akumugwira nkono.

"I know sindimayenera kukubweresa pa public ndisanakuziwitse. But people have to know now that you are taken."
"Ndiye without my decision? Umayenera undiziwitse kaye before doing all of this!"
"Molly we are dating."
"You don't know how this will affect me Zack. Ukamachita zinthu ask me first! It's not only about me. Chilichonse I do, kuntchito zimaziwika."
"Am sorry."
"You said we are trying this not tying it."

Zack azindikira kuti walakwitsa.
"Am sorry Molly. I thought..."
"Just take me home."
"Koma titha.."
"Home."
"Okay."

Ananyamuka nkumalunjika kunali geti lotulukira kuti akakwere galimoto.

Atafika kunyumba Zack anali akumupepesabe Molly.
"Am sorry."
"Sorry will not help Zack. Just live it like that. Koma ulendo wina tell me ukamafuna kuchita zinthu. Especially zimene zingandipange affect. Definitely this is the news for people to day. Ndatopa ndi drama."
"Ndikuphikire chani?"
"Chef waphika kale."
"Zophika ineyo."
"Adye izo ndindani?"
"Tidya nthawi ina."
"It’s okay. You can cook."
"Mind to join me?"
"Ndikuthandizenso?"
"Come it will be fun."

Anayimilira nkumutsatira. Anapita kukitchen ndikusankha zoti aphike.
"We cook chicken."
"That will be great."
"Kapena umafuna china?"
"No anything is okay with me."
"Ndiye tidya chicken with?"
"Chicken and chips."
"Good idea."

Anayamba kuphika kwinako akukambilana nkhani. Zack anatenga zila ndikuswa kenako anatenga flour. Akuti azithila flour uja m'adzira anamuthila Molly kumaso.
"What !? Zack?"

Zack anayamba kuseka chifukwa kunkhope konse kunali flour.
"Ulipila."
"Sorry baby."

Molly anatenga mazila nkumuthila mutu.
"Molly sindinakuthile mazila."
"It’s even now. Ine sindinakupute. "
"Ndiye mpaka mazira?"
"Ukufuna ndi bweze? Just wait waziyamba wekha."

Zack anatenga madzi amene anali nkapu nkumuthila nawo. Zack anayamba kuseka. Molly anakatenga juice mu fridge.
"No!" Anatero Zack akuthawa. Anayamba kuthamangisana mpaka Zack anathilidwa ndi juice.
"Now am satisfied."
"The juice was cold Molly!"
"Ah... i didn't know." Anatero kenako anamusiya pompaja iye nkumapita kuchipinda chake kuti akasithe.

Zack anamutsatira. Anamupeza akuvula zovala.
"Sorry." Anatero nkuzatembenuka kuti asamuone.
"Timagogoda. That's the function of the door."
"Am sorry."
"Ndikufuna ndikasambe. Sindingakhale chonchi. Mind to join me?"
"That's tempting."
"Trying my luck."
"You have failed."

Molly anaseka.
"You can use the other room. Lucky kuli zovala zachimuna. Usankha konko."
"Zovala zachimuna ukutani nazo?"
"Za Rod. Mbuyo kwambiri amabwera kuno ndiye panopa anachepetsa. Ndizovala zake."
"Ah, okay."
"Kasambe. Ukumveka mazira."
"Iwenso kasambe, nkhope yako sikuoneka bwino."
"You are insulting me."
"You started first."
"Let me ignore you."
"That will help." Anatero akumwetulira.
"Am not loosing."
"Are you?"

Anapukusa mutu nkupita kubafa. Zack anamwetulira nkupita chipinda china chija.

Pamene amatha maola atatu nkuti nyumba muja antchito atakonzamo. Zack anali atamusamira Molly pamene Molly anali atakhala pasi koma akuonera film.
"This is good."
"You like it?" Anafusa Zack.
"I do."
"How are you feeling?"
"Free."
"Free?"
"Yes."

Anayamba kuseweresa chibwano cha Zack.
"Am happy that am making you to feel free."
"Is it supposed to be like this?"
"Chani?"
"Relationships?"

Zack anakhala chete nkuzakhala bwinobwino kenako anamuyang’ana Molly.
"The problem is that people think relationship is s*x."
"That's true."
"No it's not. You have to be free from your partner. Understand one another. Trying to like what the other like even when you hate it."
"Hhhha!"
"Intimacy is a deep connection. Deep conversation. Speaking from the heart and telling one another nonsense."

Molly anamwetulira.
"Nonsense?"
"Yes."
"I can't say nonsense."
"To your partner you do koma sumazindikira kuti you are telling nonsense."

Anayang'anizana kwakanthawi kenako Molly anavomera.
"Relationship should not break you but build you."
"Why are you saying all this words?"
"You should know you worthy Molly. You are not cheap. Your the precision jewelry that is rare."
"You are sweet with words."
"Can I kiss you?"

Anayang'ana milomo yake nkuzamuyang'ana maso.
"This words are better than the kiss you want."
"Kamozi."
"No."

Zack anaseka kenako anapitiliza kuonela film. Molly amaona ngati amukakamiza.
"You gave up?"
"I respect your decision my dear. Sindingakukakamize kuchita zimene sukufuna."
"Wow."
"Bwanji?"
"Ukufuna undibere chani Zack?"
"Ndatani?"
"You are too perfect."
"Meaning?"
"I invited you to shower with me unakana and now you are not forcing me to kiss you."
"Umafuna nditani Molly?"
"I mean... nothing."
"So be it."

Comment...

10/06/2026

THE MANIPULATED QUEEN

Chapter 120

Kunyumba kwa Solo zinthu zimayipilabe. Anasiyilatu kumulabadira Solo.

Tsiku lina akudya pakhomo panamveka kugogoda nthawi imeneyo nkuti Solo ali pabalaza.

Anatsegula chitseko.
"Femi?"
"Hey."
"What are you doing here?"
"I missed you honey. I couldn't sleep."
"Femi this is my house and my husband is home."
"Koma chilipo chimene angachite?"

Anatero akumukumbatira ndikumupangisa kuti azilowa nyumba.
"What can he do."
"Izi zimayenera zikhale za private."
"Kwa ena koma not to him. Akuyenera kuziwa kuti there is someone who is helping him kuti nyumba yake iyimebe." Anamupatsa kiss.

Solo anali akuonerera zonse zimene amachita.
"I miss you."
"I miss you too."
"Dzulo ananyamuka mwachangu and sumayankha foni yanga."
"Unachita zobowa."
"Taking care of you ndizobowa?"
"You know mamuna wanga was home. I was supposed to take care of him and you did let me sleep over kenako tsiku lonse kumandikakamira."
"That's so sweet kukuona utakwiya. Complain so much."
"You see?"
"Sukufuna morning message?"
"Mmm will it be good?"
"Let's do it. You will tell me later."
"Come."

Anagwira nkono wake nkumalowera naye kuchipinda chimene amagona ndi Solo.

Solo amangomva phokoso. Anali atazazidwa ndi nkwiyo kwambiri. Analakalaka atadzukapo koma thupi lake limakana. Anali ndi nkwiyo osaneneka mpaka thupi lake linasuntha. Misozi inatsika.
"Je..... Jes..."

Anakwanitsa kusuntha koma sizinathele patali. Solo analakalaka kuzipha chifukwa cha phokoso limene limachitika.

Pamene ola limodzi limadusa wantchito anatulukira atanyamula jumbo. Naye anachita kudabwa mpaka anamuyang’ana Solo momumvera chisoni.

Anathamanga nkumuthandiza kukhala bwinobwino. Amatha kuona kuti Solo amapuma mwamphuma.

Sipanatenge nthawi Jessica ndi Femi anatuluka kuchipinda kuja akuseka. Femi anali atavala kabudula pamene Jessica anali atavala towel. Anafika pabalaza paja atachita kugwirana mwachikondi.

Anakumanizana ndi wantchito uja.
"Wagula zimene ndinakutuma?"
"Eya."
"Good, lero you are off. And zimene wawona tell no one. Got it?"
"Yes."
"Good."

Wantchito uja ananyamuka nkumapita.
"Let's go and cook. Paja umati uli ndi njala." Anatero Jessica atagwira nkono wa Femi.
"Yes but change of plan."
"Chaninso?"
"I want him to see us."
"Who?" Anatero akumuloza Solo.

Jessica anamuyang’ana Solo ndipamene amakumbukira kuti pali Solo.
"No zimene tachitazi it's enough Femi. You being half necked pamaso pake is enough."
"Look Jessica. I want to show him how i do it to you."
"Zimenezo ndi zolakwika. I know you want to prove a point koma pamaso pake? This man did lots of things to me. He loved me and I can't do it."
"Who is good when it comes to touch you. Me or him?"
"Femi please."
"Answer me Jessica. Who makes you to forget everything. Me or him?"
"I don't like this comparison."
"Koma yankho ulinalo baby. Tell me. Sangachite chilichonse. What if akunamizilanso apa. He will see and listen basitu. And you will get the credit."
"Sindikufuna."
"Jessica..."
"I can do anything but not do that to him. Akakomoka or something? I will be the one to blame."
"Sapanga chilichonse."

Anamusiya nkumapita ku kitchen.
"Are you following me or uzangokhala pamenepo or unditsatira?"
"Ndikubwera."

Pamene pamatha ma ola atatu Femi anakakonzeka nkumapita kunyumba kwake.

Solo anali atakhala pa mpando pompaja koma thukutha lake likuoneka paliponse.

Jessica anatseka chitseko kenako anamuona Solo.
"Don't worry ndikonzamo nyumba muno."

Anakonza chilichonse nkuchibwezeletsa pamalo pake. Anatenga spray wa nyumba ndikufayilamo.
"You see. Nothing happened." Anatero ndikupita kuchipinda chake.
.....

Molly kutacha anakomzeka nkupita kunyumba kwa Rod.

Anamupeza akufuna azipita ku ntchito.
"Happy birthday!"
"Molly."
"Lero sukupita ku ntchito. We are going out. "
"I just told you koma sindinati uzasokoneze tsiku langa."
"And am not here to disturb you. Am here to celebrate."
"Kodi ulibe zochita? Umayenera ukhale ku ntchito. "
"No chifukwa ndi birthday yoko."
"Molly ndachedwa."
"And am serious kuti sukupita ku ntchito."
"Molly?"
"Try me."
"This is serious I guess."
"Very serious."

Anayang'ana galimoto yake.
"Ndiye ndingoyimba foni."
"Okay."

Analankhula ndi assistant wake.
"Done." Anatero akumuonetsa foni.
"So lili sis. What have you planned?"
"A biggest surprise. Okay, mm tingalowe nyumba mwako?"
"Sure."

Anakalowa nyumba. Molly anakazithilira juice nkukhala moyang'anizana ndi Rod.
"Ndiye tiyenda motani? Birthday's are supposed to be surprises."
"Ndikuziwa." Anayankha akusiya juice wake patebulo.
"I have this friend of mine. Ndi best friend wanga more like a sister. Lero ndi birthday ya mwana wake. So you and the child are plus one today."
"Okay."
"Ndikamwana kokongola. Ndimayenera kuti ndipite as you know she is my friend."
"Ndikukumva."
"And Iwenso you are celebrating so it's double celebration."
"Mmmh."
"The baby will be 5. Dzina lake ndi Lisa. And her mother...." Anamuyang’ana Rod uja.
"Bwanji?"
"I know ukango ona the mother you will definitely love her. "

Rod anaseka.
"Zimene ndikunenazi Rod ndi zenizeni. I know your type. Nkazi amene ungamukonde sikuti ndi nkazi wamba. She is the best of the best. "
"Ukuziwa chimene chikundisangalasa ndi chani?"
"No."
"You are so sure that I would like this lady. Molly wekha wanena kuti she has a child. That means ali ndi mamuna. And ineyo am still thinking about Stella. Sindinasiye and I will not stop-"
"Okay I got this. Mapeto ake tizingotsutsana tsiku lonse. So Rodney, tikadyera limodzi birthday imeneyi kwa nzanga."
"Ngati ndizimene ukufuna so be it."
"Chilichonse ndakonza kale. Iweyo ukangolongeza zinthu zako zochepa chabe."
"Zinthu ngati chani?"
"Zovala. Uzifuna kumene tikupitaku."
"Tikakhala masiku angati kodi. Mesa ndi birthday kenako tizikabwera."
"Just do what I told you."

Anamuyang’ana Molly uja kenako anapita nkukalongeza zofunika. Pamene amalongeza nkuti Molly akuyimbira driver wake kuti azamutenge.

Anamuyimbira Lucas foni ndikumuziwise zoti sakhalapo kwa masiku angapo.
"It’s okay. Ndisamalila chilichonse."
"Thanks."

Ndipamene Rod amatulukira atatenga chikwama chake.
"Chokhacho?"
"Umafuna chikhale chachikulu?"
"Bola usanene kuti sindinakuwuze."
"Pafunika zambiri?"
"Ayi zochepa. Tiye."

Anatuluka panja ndikumakadikira. Rod anatseka chitseko. Analankhula ndi geti mani kenako anatuluka kunja ndikumakadikira.
"Tikanatha kukwera galimoto yako."
"Ndizatenga ndikabwera. Ili safe konkuno."

Galimoto inafika ndikuwatenga. Inakawasiya kumene kunali ndege za Akron group. Anakakwera helicopter. Rod anayamba kukhala ndimafunso.

"Ndiye wati nzako ameneyu ndi ndani? Ndimangoziwa Becca ekha."
"Becca timacheza chifukwa she is my doctor. A good one. "
"Ndiye who is this one. And on top of that she has a child. Sindikuziwa nzako wina aliyense amene ali ndi mwana."
"Ndiye ndiyankhe chani pamene? Rod sungaziwe anzanga onse."
"Koma umaziwa anga."
"That's it. Ndife osiyana."
"Okay mwina ndafusa molakwika. Can you tell me more about this friend of yours."

Molly anamuyang’ana.
"Mbuyomu analuza memory. Koma pachiyambi she had a good family. A good man to speak of. She loved him so much to the point yofuna kupereka moyo wake."

Rod anameza malovu.
"Koma mwamway. She lost her memory. Anaiwala za mamunayo komanso sizokhazo. She was pregnant for the man."
"That's sad."
"Really sad."
"Ndiye amakhala kuti?"
"Panopa amakhala mudzi wina wake. She is happy with he baby girl."
"And the man?"
"I don't know Rod."

Rod anakhala chete nkumamvetsera. Ntima wake umagunda mwachilendo. Amangokumbukira zimene Molly analankhula.
"Koma ndiye ndikutalitu."
"Tasala pang'ono."
"Mpaka birthday yanga ithera mu ndege muno."
"No. Tangoyambapo."

Atatsika ndege ija panali galimoto yoti iwatenge.
Asanakwere Molly anagwira nkono wa Rod.
"Promise me something."
"Chani?"
"That you will behave."
"You are scaring me."
"Just control your emotion. My friend doesn't know you. Ukumbukire zimenezo. She doesn't know you."

Rod anaseka mwa mwantha.
"Ndikuziwa kuti samandiziwa."
"Take that. Tiye."
Anakakwera galimoto ija.

Mugalimoto aliyense analichete osalankhula ndi nzake. Anafika ku restaurant imene imawoneka kuti munali anthu koma ochepa. Rod anakatsitsa ekha chikwama pamene Molly anachita kutsitsilidwa ndi driver.

Anayima pa nsewu onse akuyang'ana ku restaurant kuja.
"Remember I told you she doesn't know you."
"Wanena zimenezo kochuluka."
"Just remember."

Analunjika ku restaurant kuja. Atangolowa Molly anayang'ana kumene kunali Stella. Sipanatenge nthawi anatulukira atatenga mbale ndikukasiya patebulo ina.
"Stella." Anayitana Molly Ndipamene Stella amawachewukira.

Anamuona Molly uja.
"You are here. " Anatero akumwetulira. Anapita pamene anayima Molly uja.
"Thank you for coming."
"Happy birthday."
"Ndi birthday ya Lisa not mine."
"I know.... meat my brother, we are here to celebrate."

Nthawi yonse imene amakambirana Rod anangoyima ngat chikwangwani asakugwedera. Molly atasuntha ndipamene Stella anazindikira kuti anali ndi munthu ndipo munthu winayo sanali wina koma....

Anayang'anizana aliyense akumudabwa nzake.
"Rod?"
"Stella.."

Comment...

Want your business to be the top-listed Government Service in Lilongwe?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Website

Address

The Email And Phone Number Will Do
Lilongwe