26/10/2026
BOMA LATSEGULA CHIPATALA CHATSOPANO CHA MAKANJIRA
Boma lati dziko la Iceland ndi bwenzi lenileni pa chitukuko.
Poyankhula pa mwambo wotsegula Chipatala chatsopano cha Makanjira Lolemba, Nduna ya maboma ang'ono ndi chitukuko cha Kumidzi, Dr Ben Malunga Phiri, yati ntchito zomanga zomwe Iceland yathandiza ku Mangochi zithandiza kwambiri kupititsa patsogolo ntchito zotukula miyoyo ya anthu.
A Phiri ati chipatala chatsopanochi, chomwe chamangidwa ndi ndalama zoposa K2.4 biliyoni, chithandiza amayi oyembekezera ndi ana obadwa kumene kupeza chithandizo mwachangu, komanso kuchepetsa imfa, m'madera ovuta kufikako a Makanjira, Lulanga ndi ena ozungulira.
"Chipatalachi chichepetsa mavuto omwe anthu akukumana nawo pofuna chithandizo, pomwe ena ankayenda mtunda woposa makilomita 100 kukafuna chithandizo.
"Ichi ndi chitukuko choyamikirika, ndipo ndikuthokoza boma la Iceland chifukwa chothandizira boma. Kuyambira chaka cha 1964, Iceland yakhala bwenzi lathu lodalirika," atelo a Phiri.
Pa nkhani ya misewu, a Phiri atsimikizira anthu ku Mangochi kuti boma likukonza misewu.
Iwo ati padakali pano, boma layamba kukonza msewu wa Makanjira pomanganso milatho ikuluikulu isanu ndi inayi (9), kudzera mu pulogalamu ya Regional Climate Resilience.
Poyankhula, Mtsogoleri wa za Chitukuko cha Mayiko mu Unduna wa Zakunja ku Iceland, Mimi Soebeth, yati boma lake lasangalala ndi kumaliza kwa chipatalachi, ndipo ali ndi chikhulupiliro kuti chipatalachi chisintha kwambiri kayendetsedwe ka ntchito za umoyo.
Mmawu awo, mfuyu yayikulu Makanjira wayamika boma chifukwa choganizira anthu ake.
District Council
wa bwino kwa anthu