03/06/2026
SHORTLISTED CANDIDATES FOR THE POST OF TEMPORARY REGISTRATION ASSISTANTS
Mchinji District Council would like to invite shortlisted candidates for the post
of Temporary Registration Assistant to attend written interviews which have been
scheduled as follows:
VENUE: Mchinji Teachers Training College
DATE : 5th June, 2026 (Friday)
TIME : 7:30 AM
NOTE: All the candidates are requested to bring original ceftificates, National
Identity Card, and writing materials.
28/05/2026
Khonsolo ya Mchinji lero ikukhazikitsa lamulo lomwe mtsogoleri wa dziko lino anakhazikitsa losamalira malo ndi ukhondo mmalo omwe akukhala komanso kuchitira malonda.
Mwambowu ukuchitikira ku Kapiri komwe khonsoloyi motsogozedwa ndi bwanankubwa Reinghard Chavula, akusesa mu msika komanso malo ozungulira Trading Centre yi.
Mfumu yaikulu Dambe, wapampando wa khonsolo a Kennedy Chipanga, wamkulu wa polisi a Dr David Kumwenda, akuluakulu a za umoyo, ochita malonda, akuluakulu a mabungwe omwe si aboma, akulu akulu a banki ya Centenary, ogwira ntchito mu boma komanso achinyamata anatenga nawo gawo.
Prof. Arthur Peter Mutharika, anayika lamulo loti malo onse aboma, okwerera mabasi, misika, ndi malo ogwirira ntchito akhale ndi zida zothandizira ukhondo. Cholinga cha lamuloli ndi kuteteza anthu ku matenda monga kolera.
Mwachidule, lamulo li likuti malo aboma ndi misika, malo okwerera mabasi, malo oyima galimoto (car parks), ndi malo ena onse okhala anthu ambiri ayenera kukhala ndi malo abwino otayira zinyalala komanso malo ogwirira ntchito ndi masukulu aboma ndi a private komanso malo ogwirira ntchito ayenera kukhala ndi zida zothandizira ukhondo ndi zotayira zinyalala.
Ma khonsolo ndiponso ma bungwe azaumoyo ayenera kuonetsetsa kuti lamuloli likuyenda.
14/05/2026
Achinyamata amakhala otakataka...Achinyamata youth network ya kwa Zulu mmawa wa pa 14 May anali kalikiliki kusesa ndi kukonza ku chipatala chachikulu cha Mchinji.
Mogwirizana ndi Space4Youth and Zikomo Social Net achinyamata a Zulu Youth Network wa agwira ntchito yotamandika pofuna kuonesetsa kuti ka chipatala kwathu kuli ukhondo.
Mkulu oyang'anira achinyamata ku Mchinji a Ian Sukali ayamikira achinyamata wa ponena kuti izizi zikuonetaeratu poyera kusintha kwa kaganizidwe pamene achinyamata akuyikidwa patsogolo molunjika Malawi 2063.
Zulu Youth Network
Zikomo Social Net
Space4Youth Business Hub
14/05/2026
Happy Kamuzu Day...14th May!
08/05/2026
Mu nkhani zina.... Banki ya Centenary yathandiza khonsolo ya Mchinji ndi zipangizo zogwiritsa ntchito posamalira malo osiyansiyana.
14/04/2026
CHIDZIWITSO
MITENGO YOYAMBIRA KUGULA MBEWU MU CHAKA CHA 2025/2026
Unduna wa Malimidwe, Ulimi Othilira ndi Chitukuko cha Madzi ukudziwitsa anthu onse m'dziko lino za mitengo yogulira mbewu ya chaka cha 2025/2026.
Onse ogula mbewu akuchenjezedwa kuti kugula mbeu kwa alimi pa mitengo yotsikilapo pa imene yakhazikitsidwayi ndi mlandu waukulu ndithu.
Chiphaso chogulira mbewu mukhoza kukatenga ku maofesi owona za ulangizi wa mbewu omwe ali kuseli kwa Natural Resources College kapenanso kumaofesi onse a Agricultural Development Division (ADD) a Karonga, Mzuzu, Kasungu, Salima, Lilongwe, Machinga, Blantyre ndi Shire Valley.
03/04/2026
Pasaka yabwino kwa nonse kuchokera kuno ku khonsolo ya Mchinji!
25/03/2026
Tikakhomere ziphaso zathu za bizinesi. Tidziwitsenso kuti pakali pano pakuchitika kalembera wa ma bizinesi!