14/03/2026
Pulezidenti Peter Mutharika wanena kuti iye ali kumbuyo kwa Komiti yoona zosankha anthu maudindo a boma ku parliament(PAC) yomwe ikufufuza pazakugulitsidwa kwa hotelo ya Amaryllis kupyolera mu ndalama zomwe zimasungidwa ndi bungwe loona za anthu ogwira ntchito m'boma.
Mutharika wati iye akutsatira nkhaniyi mwachidwi ndipo aonesesa kuti chilungamo chitsatidwe.
Komitiyi Khalapampando wake ndi Baba Steve Malondera.
Inuyo mukutipo bwanji? Kodi APM wabwera panthawi yake yomwe amafunika kutero kapena akanadikira kaye aone chitsogolo chake?
24/02/2026
TIMVE KWA INU👂👂👂
Akuti President Mutharika walamula kuti pakuyenera kuchitikanso kafukufuku wina pa zomwe zinachititsa kuti ndege yomwe anakwera yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino igwe ndikupha anthu 9 omwe ndikuphatikizapo Wachiwiri kwa mtsogoleriyu a Saulosi Chilima.
Inu mukuona kuti ndi zofunikadi kutero kapena ayi?
23/02/2026
Dziko la Malawi lakhala pa nambala 8 pokhala dziko lomwe likulamuliridwa bwino muno mu Africa. Dzikoli lakhala pa nambala 71 pa dziko lonse lapansi.
Izi zikuchitika patangopita miyezi yochepa President Peter Mutharika atangotenga kumene mpando wautsogoleri wadziko lino.
Tiuzeni ndemanga yanu pankhaniyi..
26/10/2025
Ntchito iyambike pa ground tsopano.